Pakati Song Lyrics
Pakati by Langwan Piksy VERSE ONE
Pakati, pa kuwala ndi mdima
Pakati, pakutentha ndi kuzizira
Pakati, pa chubu ndi mpira
Pakati, pa nkhuku ndi dzira
Nkakhala ofunda mudzandilavula
Sinfuna kulavulidwa
Sinfuna kulavulidwa
Ndiri ngati munda wosalambula
Ndifuna kupaliridwa
Ndifuna kupaliridwa
CHORUS
Mundiike kumene mufuna
Mundiike kumene mufuna
Kuti zonse zomwe ndichita
Zisangalatse inu
Mundiike kumene mufuna
Mundiike kumene mufuna
Kuti zonse zomwe ndichita
Zisangalatse inuyo
VERSE TWO
Pakati, pa mbuzi ndi gwape
Pakati, pa galu ndi nkhadwe
Pakati, pa dzulo ndi lero
Pakati, pa usiwa ndi ulemelero
Nkakhala ofunda mudzandilavula
Sinfuna kulavulidwa
Sinfuna kulavulidwa
Ndiri ngati munda wosalambula
Ndifuna kupaliridwa
Ndifuna kupaliridwa
CHORUS
Mundiike kumene mufuna
Kumene mufuna
Kuti zonse zomwe ndichita
Zisangalatse inu
Kumene mufuna
Mundiike kumene mufuna
Kuti zonse zomwe ndichita
Zisangalatse inuyo
VERSE THREE
Sindziwa za mawa
Tsono ndikhala ndi nkhawa
Ndikhala moyo wa mantha
Njira yanga iwunikidwe
Odziwa za ku mwamba
Akuti ndiri nziwanda
Ndikhala moyo wa mantha
Ndingatani ndimasulidwe
Ndingatani ndimasulidwe
Ndiri pa katiiii
CHORUS
Mundiike kumene mufuna
Kumene mufuna
Kuti zonse zomwe ndichita
Zisangalatse inu
Kumene mufuna
Mundiike kumene mufuna
Kuti zonse zomwe ndichita
Zisangalatse inuyo